News in English

Kulira kwake ndiye nkumatani abale?- UTM

Chipani cha UTM chati imfa ya Soldier Lucius Banda mnjowawa kwambiri maka pomwe chipanichi chikulirabe mtsogoleri wawo a Saulos Chilima. Banda anali mkulu okopa (Campaign Director pachingerezi) anthu mchipani cha UTM. Mneneri wa UTM a Felix Njawala wati ngati chipani sakudziwa kuti nkumatanino ndi momwe imfa yatengera akuluakulu ake motsogozana. “Pomwe a Chilima ankachokera ku […]

The post Kulira kwake ndiye nkumatani abale?- UTM appeared first on Malawi Voice.

Chipani cha UTM chati imfa ya Soldier Lucius Banda mnjowawa kwambiri maka pomwe chipanichi chikulirabe mtsogoleri wawo a Saulos Chilima.

Banda anali mkulu okopa (Campaign Director pachingerezi) anthu mchipani cha UTM.

Mneneri wa UTM a Felix Njawala wati ngati chipani sakudziwa kuti nkumatanino ndi momwe imfa yatengera akuluakulu ake motsogozana.

“Pomwe a Chilima ankachokera ku South Korea posachedwa, adadzera ku South Africa kukamuona Lucius Banda.

“Akuluakulu a chipani angapo akhalanso akukamuona. Sitinaganize kuti zithera chonchi. Kulira kwake ndiye nkumatani abale?” a Njawala awuza Times 360.

The post Kulira kwake ndiye nkumatani abale?- UTM appeared first on Malawi Voice.

Читайте на 123ru.net