News in English

Lazaro wagwera m’chimbudzi

Bambo wina yemwe akuti dzina lake ndi Mavuto Lazaro athamangira naye ku chipatala cha Kasungu, atagwera m’dzenje lomwe akumba kuti chikhale chimbudzi pa mzikiti wa Chitete m’bomali. Sheikh Amdan Omar wati akuganiza kuti bamboyu anagwera m’dzenjero usiku wapitawu chifuwa anthu amuonamo m’mbanda kucha walero. A Omar ati atamufunsa, bamboyu anakwanitsa kungotchula dzina lakelo ndi kuti […]

The post Lazaro wagwera m’chimbudzi appeared first on Malawi Voice.

Bambo wina yemwe akuti dzina lake ndi Mavuto Lazaro athamangira naye ku chipatala cha Kasungu, atagwera m’dzenje lomwe akumba kuti chikhale chimbudzi pa mzikiti wa Chitete m’bomali.

Sheikh Amdan Omar wati akuganiza kuti bamboyu anagwera m’dzenjero usiku wapitawu chifuwa anthu amuonamo m’mbanda kucha walero.

A Omar ati atamufunsa, bamboyu anakwanitsa kungotchula dzina lakelo ndi kuti amachokera ku Chiphaso, m’bomali, kotero iwo apempha anthu omwe angadziwe bamboyu kuti akanene ku polisi.

Ena mwa anthu omwe anathandizira kutulutsa bamboyo m’dzenjemo, ati akuganiza kuti bamboyu analedzera.

The post Lazaro wagwera m’chimbudzi appeared first on Malawi Voice.

Читайте на 123ru.net