News in English

Manganya ndi kape kwambiri – Winiko

Katswiri wodziwika bwino pa nkhani za zisudzo m’dziko muno a Winiko ati Manganya ndi “kape kwambiri” ndipo “azamupasa makofi”. Winiko, yemwe anabadwa ndi dzina la Bon Kalindo ndipo wakhala akupanga masewero ndi Manganya, wayakhula izi pa pologalamu ya padera yomwe yaulutsidwa pa wayilesi ya Zodiak Lachiwiri madzulo, “Manganya ndi kape kwambiri, pali sewero lina lake […]

The post Manganya ndi kape kwambiri – Winiko appeared first on Malawi Voice.

FILE: Winiko (Centre)- Manganya ndi kape kwambiri

Katswiri wodziwika bwino pa nkhani za zisudzo m’dziko muno a Winiko ati Manganya ndi “kape kwambiri” ndipo “azamupasa makofi”.

Winiko, yemwe anabadwa ndi dzina la Bon Kalindo ndipo wakhala akupanga masewero ndi Manganya, wayakhula izi pa pologalamu ya padera yomwe yaulutsidwa pa wayilesi ya Zodiak Lachiwiri madzulo,

“Manganya ndi kape kwambiri, pali sewero lina lake lomwe ndinapanga naye ndipo musewero mo anabwera kwa ine pamodzi ndi dzukulu  wang, ndipo anandinamiza kuti iye ndi mkazi,” anatero a Winiko

Malingana ndi a Winiko, Maganya wakhala akuwaputa dala mumasewero ambiri omwe awiri-wa akhala akupangira limodzi, pamenepa iwo anabwereza kunena kuti: “ Manganya ndi kape, ndizamuswa”.

Ku mbari ya dziko, a Manganya omwe anabadwa ndi dzina la Micheal Usi ndi achiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino komanso ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM.

Malingana ndi a Kalindo, Manganya ndi munthu opanda nzeru pomwe Usi ndi munthu wa nzeru oganiza bwino, ponena kuti ali ndikuthekera kutukula dziko lino.

Awiri-wa akakhala akupangira limodzi sewero la Tikuferanji?, lomwe lakhala likuwonetsedwa pa kanema ya MBC komanso Times kwa zaka zingapo tsopano.

Ndipo poyakhulapo pa momwe dziko likuyendera, a Kalindo omwenso ndi omenyera ufulu wa anthu, anati i zithu zambiri ndizosokonekera kamba koti dziko lino linapita kwa “agalu”.

Pogwira mawu a Kalindo, atsogoleri onse omwe alamulirapo dziko lino anayesa kuyika patsogolo umoyo wa anthu zomwe ati pano sizikuchitika.

“Nthawi ya Bakili Muluzi kunali starter pack, nthawi ya Bingu wa Mutharika kunali feteleza otchipa, nthawi ya Joyce Banda anayesetsa, Peter Mutharika nayenso anayesetsa kumbali yake. Nthawi imene ija mafuta a galimoto anali pa mtengo otsikilako koma awawa akuoneka ngati anali pa ludzu nthawi yaitali.

“Khoswe akamaluma munthu amapepelera munthuyo osadziwa kuti akulumidwa, koma awawa eee! Ndikufuna ndibwerezenso mopanda mantha; dzikoli lapita kwa a galu ndipo panakakhala mwayi woti anthu asamuke, m’Malawi muno mukanatsala a Chakwera okha ndi abale awo, ambiri akanasamuka chifukwa akuvutika,” anatero a Kalindo.

A Kalindo ati amayembekezera kuti chipani cha Malawi Congress (MCP) chipanga zodabwitsa pa zaka zisanu zoyambilira, zomwe ati sizikuchitika. Bambo Kalindo ati pano andale kukacha akumaganiza kuti kodi apanga ndalama zingati zoti azitumize kunja.

Iwo adandaulanso kuti pansi pa ulamuliro wa MCP ndalama ikusowa kwambiri m’dziko muno zomwe wati zapangitsa a Malawi ochuluka kukhala pa umphawi wa dzaoneni pamene atsogoleri andalewo akulemera mododometsa.

“Munthu wakumudzi amangofuna akhale pa ntchito akhale pa bizinezi yabwino, koma andalewa amapanga dala ndi kuyamba kusowetsa ndalama monga m’mene apangira awa a MCP asowetsa ndalama m’dziko muno kuti anthu adzipita kwa iwo kukawapempha kuti iwo adzioneka ngati ndi milungu,” watelo Kalindo.

Kalindo anayankhula mokuluwika ponena kuti atsogoleri anzeru amatenga mafupa ndikumupatsa a galu kuti iwo azidya bwino minofu, ndipo ati nzodabwitsa kuti kuno andale akudya mafupa ndi minofu yomwe okha, kuwasiya anthu ali pa dzuwa.

The post Manganya ndi kape kwambiri – Winiko appeared first on Malawi Voice.

Читайте на 123ru.net