Chaka cha mawa ndiyambapo ntchito yokonza Malawi- Mutharika watsimikizira Mafumu a ku Machinga
Mtsogoleri wa chipani cha Democtratic Progressive (DPP) a Professor Arthur Peter Mutharika alonjeza kuti chaka cha mawa akalowa m’boma azakonzanso zina mwa zinthu zomwe zasokonekela pansi pa ulamuliro wa a Lazarus Chakwera.
A Mutharika, omwenso ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino, wanena izi pa mbuyo pa m’kumano omwe anali nawo ndi mafumu a m’boma la Machinga.
Malingana ndi a Mutharika, pa mkumanowu, mafumwa anadandaula kuti zinthu sizili bwino.
“Anandidandaulira za mavuto amene akukumana nawo monga aMalawi onse mu utsogoleri ulipowu. Ndawatsimikizira kuti chaka chamawa ndikalowa m’boma ndiyambapo ntchito yokonza mavuto amenewa kuti moyo wawo uyambirenso kusintha,” atero a Mutharika
Iwo anawonjezera kuti akuziwa bwino lomwe za mavuto monga kukwera mitengo kwa zinthu, kufinyika kwa anthu a bizinesi zing’ono zing’ono, kusowa kwa chitetezo ndi mavuto ochuluka.
“Koma musataye chikhulipiliro a Malawi, 2025 ndikubweranso. Tikhonza zinthu,”
Mafumu pamodzi ndi anthu ena anatsogozedwa ndi phungu wa dera la pakati cha ku m’mawa kwa boma la Machinga, a Daud Chikwanje
The post Chaka cha mawa ndiyambapo ntchito yokonza Malawi- Mutharika watsimikizira Mafumu a ku Machinga appeared first on Malawi Voice.