Musaope ngongole, mukaopa muzagona ndi njara- MCP yauza a Malawi omwe akukutika ndi umphawi
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) a Catherine Gotani-Hara ati anthu asamaope kutenga ngongole ya NEEF.
A Hara ayankhula izi pa bwalo la St. Martin’s ku Zomba Thondwe lero Lamulungu pa msonkhano wa ndale.
Malingana ndi a Gotani Hara, omwenso ndi sipikala wa nyumba ya malamulo, ngongole ya NEEF ndi ya Amalawi eniake, chomcho asawope kukatenga.
Pamenepa, mayi Gotani Hara ati aonetsetsa kuti adindo atengepo gawo pothandiza Amalawi kutenga ngongolezi.
Pa nkhani ya njara yomwe yafipa povuta m’dziko muno, a Gotani-Hara, atsimimikizira anthu aku Zomba kuti alandira chimanga.
M’mawu awo, a Gotani-Hara atinso mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwera, akufuna dziko lino likhale ndi chakudya chochuluka.
Iwo ati, ichi ndi chifukwa chake boma la a Chakwera laakhazikitsa ntchito za ma Mega Farms pofuna kukwaniritsa izi.
The post Musaope ngongole, mukaopa muzagona ndi njara- MCP yauza a Malawi omwe akukutika ndi umphawi appeared first on Malawi Voice.